Daniel 1:5 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inawaikira gawo la chakudya cha mfumu tsiku ndi tsiku, ndi la vinyo wakumwa iye, ndi kuti awalere zaka zitatu, kuti potsiriza pake aimirire pamaso pa mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mfumu imawapatsa tsiku ndi tsiku gawo la chakudya ndi vinyo wa ku nyumba yaufumu, ndi kuti awaphunzitse kwa zaka zitatu, ndipo kenaka adzayambe kutumikira mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inawaikira gawo la cakudya ca mfumu tsiku ndi tsiku, ndi la vinyo wakumwa iye, ndi kuti awalere zaka zitatu, kuti potsiriza pace aimirire pamaso pa mfumu.