Daniel 10:12 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anati kwa ine, Usaope Daniele; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iye anapitiriza nati, “Usachite mantha Danieli. Kuyambira tsiku loyamba pamene unatsimikiza mtima kuti umvetse zinthuzi ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, pempho lako linamveka ndipo ndabwera kudzayankha mapemphero akowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anati kwa ine, Usaope Danieli; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzicepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako,