Daniel 10:3 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chakudya chofunika osachidya ine, nyama kapena vinyo zosapita pakamwa panga, osadzola ine konse, mpaka anakwaniridwa masabata atatu amphumphu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sindinadye chakudya chokoma; nyama ndi vinyo sizinakhudze milomo yanga ndi pangʼono pomwe; ndipo sindinadzole mafuta aliwonse mpaka patatha masabata atatu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cakudya cofunika osacidya ine, nyama kapena vinyo zosapita pakamwa panga, osadzola ine konse, mpaka anakwaniridwa masabata atatu amphumphu,