Daniel 10:6 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
thupi lake lomwe linanga berulo, ndi nkhope yake ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ake ngati nyali zamoto, ndi manja ake ndi mapazi ake akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ake kunanga phokoso la aunyinji.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Thupi lake linali ngati mwala wonyezimira, nkhope yake ngati chiphaliwali, maso ake ngati muni wowala, manja ndi miyendo yake ngati mkuwa wowala, ndipo mawu ake ngati liwu la chikhamu cha anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
thupi lace lomwe linanga berulo, ndi nkhope yace ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ace ngati nyali zamoto, ndi manja ace ndi mapazi ace akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ace kunanga phokoso la aunyinji.