Daniel 11:17 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzalimbitsa nkhope yake, kudza ndi mphamvu ya ufumu wake wonse, ndi oongoka mtima pamodzi naye; ndipo adzachita chifuniro chake, nadzampatsa mwana wamkazi wa akazi kumuipitsa; koma mkaziyo sadzalimbika, kapena kuvomerezana naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Idzafika ndi mphamvu za ufumu wake wonse ndipo idzayesa kuchita pangano la mtendere ndi mfumu ya kummwera. Ndipo idzamupatsa mwana wake wamkazi kuti amukwatire ndi cholinga cholanda ufumu, koma zolinga zake sizidzatheka kapena kumuthandiza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzalimbitsa nkhope yace, kudza ndi mphamvu ya ufumu wace wonse, ndi oongoka mtima pamodzi naye; ndipo adzacita cifuniro cace, nadzampatsa mwana wamkazi wa akazi kumuipitsa; koma mkaziyo sadzalimbika, kapena kubvomerezana naye.