Daniel 11:18 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pambuyo pake adzatembenuzira nkhope yake kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwake adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka idzatembenukira ku mayiko a mʼmbali mwa nyanja ndi kulanda mizinda yambiri, koma mtsogoleri wina wa nkhondo adzathetsa kudzikuza kwakeko ndipo adzabwezera chipongwecho kwa iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pambuyo pace adzatembenuzira nkhope yace kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwace adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwace.