Daniel 11:2 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano ndikufotokozera choonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu m'Persiya, ndi yachinai idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Agriki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo tsopano ndikuwuza zoona: Mafumu ena atatu adzalamulira ku Peresiya, ndipo kenaka padzadzuka mfumu yachinayi imene idzakhala yolemera kwambiri kuposa onsewo. Popeza kuti idzakhala ndi mphamvu chifukwa cha chuma chake, idzadzutsa onse kuti alimbane ndi ufumu wa Grisi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano ndikufotokozera coonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu m'Perisiya, ndi yacinai idzakhala yoletnera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwace idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Helene.