Daniel 11:24 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzafika kachetechete kuminda yokometsetsa ya derali, nadzachita chosachita atate ake, kapena makolo ake; adzawawazira zofunkha, ndi zankhondo, ndi chuma, nadzalingiririra malinga ziwembu zake; adzatero nthawi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwadzidzidzi, iye adzazithira nkhondo zigawo zolemera kwambiri ndipo adzachita zimene makolo ake ngakhale agogo ake sanachitepo. Iye adzagawira zolanda, zofunkha ndi chuma kwa omutsatira. Adzachita chiwembu cholanda mizinda yotetezedwa koma kwa kanthawi kochepa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzafika kacetecete ku minda yokometsetsa ya derali, nadzacita cosacita atate ace, kapena makolo ace; adzawawazira zofunkha, ndi zankhondo, ndi cuma, nadzalingiririra malinga ziwembu zace; adzatero nthawi.