Daniel 11:25 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nadzautsa mphamvu yake ndi mtima wake ayambane ndi mfumu ya kumwera ndi khamu lalikulu la nkhondo; ndi mfumu ya kumwera idzachita nkhondo ndi khamu lalikulu ndi lamphamvu ndithu; koma sadzaimika, popeza adzamlingiririra ziwembu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mfumu ya kumpoto idzalimba mtima, ndipo idzasonkhanitsa gulu lalikulu la ankhondo kuti lithire nkhondo mfumu yakummwera. Mfumu yakummwera ndi gulu lake lankhondo lalikulu ndi lamphamvu idzathirana nkhondo ndi mfumu yakumpoto koma sidzapambana chifukwa cha ziwembu zimene adzamukonzera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nadzautsa mphamvu yace ndi mtima wace ayambane ndi mfumu ya kumwela ndi khamu lalikuru la nkhondo; ndi mfumu ya kumwela ndi khamu lalikuru ndi lamphamvu ndithu; koma sadzaimika, popeza adzamlingiririra ziwembu.