Daniel 11:30 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti zombo za ku Kitimu zidzafika kuyambana naye; chifukwa chake adzatenga nkhawa, nadzabwerera, nadzaipidwa mtima ndi chipangano chopatulika, nadzachita chifuniro chake; adzabweranso, nadzasamalira otaya chipangano chopatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sitima zapamadzi zochokera ku mayiko a ku madzulo zidzalimbana naye, ndipo adzataya mtima. Kenaka idzabwerera mopsa mtima ndi kudzalimbana ndi chipembedzo cha anthu opatulika. Idzabwerera ndi kuchitira chifundo amene sadzasunga pangano loyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti zombo za ku Kitimu zidzafika kuyambana naye; cifukwa cace adzatenga nkhawa, nadzabwerera, nadzaipidwa mtima ndi cipangano copatulika, nadzacita cifuniro cace; adzabweranso, nadzasamalira otaya cipangano copatulika.