Daniel 11:36 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu idzachita monga mwa chifuniro chake, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iliyonse nidzanena zodabwitsa pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzachitidwa ukaliwo; pakuti chotsimikizika m'mtimacho chidzachitika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mfumu ya kumpoto idzachita zimene ikufuna. Idzadzikweza ndi kudziyesa yopambana mulungu aliyense ndipo idzanenera za mwano Mulungu wa milungu. Iyo idzapambana mpaka nthawi yoti Mulungu ayilange mwa mkwiyo itakwana popeza chimene chatsimikizika chiyenera kuchitika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu idzacita monga mwa cifuniro cace, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iri yonse nidzanena zodabwiza pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzacitidwa ukaliwo; pakuti cotsimikizika m'mtimaco cidzacitika.