Daniel 11:37 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ake, kapena choikhumba akazi, kapena kusamalira milungu iliyonse; pakuti idzadzikuza koposa onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumuyo idzanyoza milungu ya makolo ake ndiponso mulungu wokondedwa ndi akazi, sidzachitiranso ulemu mulungu aliyense, koma idzadzikweza yokha pamwamba pa onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ace, kapena coikhumba akazi, kapena kusamalira milungu iri yonse; pakuti idzadzikuza koposa onse.