Daniel 11:4 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuuka iye ufumu wake udzathyoledwa, nudzagawikira kumphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yake akudza m'mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wake anachita ufumu nao; pakuti ufumu wake udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ufumu wake ukadzafika pachimake, udzawonongedwa ndi kugawidwa mʼzigawo zinayi. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa zidzukulu zake, ndipo olowa mʼmalo mwake sadzakhala ndi mphamvu monga anali nazo, chifukwa ufumu wake udzazulidwa ndi kuperekedwa kwa ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuuka iye ufumu wace udzatyoledwa, nudzagawikira ku mphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yace akudza m'mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wace anacita ufumu nao; pakuti ufumu wace udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai.