Daniel 11:40 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwera idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kamvulumvulu, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa nthawi yomaliza mfumu yakummwera idzachita nkhondo ndi mfumu yakumpoto. Koma mfumu yakumpotoyi idzayikantha ndi magaleta ndi akavalo ndi sitima zapamadzi zambiri ngati mphepo yamkokomo. Idzalowa mʼmayiko ambiri ndikuwakokolola onse ngati madzi osefukira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwela idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kabvumvulu, ndi magareta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.