Daniel 12:1 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa nthawi imeneyo Mikayeli, mngelo wamkulu amene amateteza anthu a mtundu wako, adzabwera. Imeneyi idzakhala nthawi ya mavuto aakulu omwe sanaonekepo kuyambira pachiyambi cha mitundu ya anthu mpaka nthawi ikudzayo. Komatu pa nthawiyi anthu a mtundu wako, aliyense amene dzina lake lidzapezeke lolembedwa mʼbuku adzapulumutsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaeli kalonga wamkuru wakutumikira ana a anthu amtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi, yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku.