Daniel 2:10 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ababiloni anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu pa dziko lapansi wokhoza kuwulula mlandu wa mfumu; chifukwa chake palibe mfumu, mkulu, kapena wolamulira, wafunsira chinthu chotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Ababiloni ali onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alawuli anayankha mfumu kuti, “Palibe munthu pa dziko lapansi amene akhoza kuchita chimene mfumu ikufunsa! Palibe mfumu, kaya yayikulu kapena yamphamvu bwanji imene inafunsapo amatsenga, owombeza kapena alawuli aliwonse zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akasidi anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu pa dziko lapansi wokhoza kuulula mlandu wa mfumu; cifukwa cace palibe mfumu, mkuru, kapena wolamulira, wafunsira cinthu cotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Akasidi ali onse.