Daniel 2:14 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Daniele anabweza mau a uphungu wanzeru kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, adatulukawo kukapha eni nzeru a ku Babiloni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Danieli anayankhula mwanzeru ndi mwaulemu kwa Ariyoki, mkulu wa asilikali olondera mfumu amene anatumidwa kukapha anthu anzeru a ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Danieli anabweza mau a uphungu wanzeru kwa Arioki mkuru wa olindirira a mfumu, adaturukawo kukapha eni nzeru a ku Babulo;