Daniel 2:15 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
anayankha nati kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, Chilamuliro cha mfumu chifulumiriranji? Pamenepo Ariyoki anadziwitsa Daniele chinthuchi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Danieli anafunsa Ariyoki kapitawo wa mfumu kuti, “Chifukwa chiyani mfumu yapereka lamulo lankhanza lotere?” Kenaka Ariyoki anafotokoza nkhaniyi kwa Danieli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
anayankha nati kwa Arioki mkuru wa olindirira a mfumu, Cilamuliro ca mfumu cifulumiriranji? Pamenepo Arioki anadziwitsa Danieli cinthuci.