Daniel 2:30 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine, chinsinsi ichi sichinavumbulutsidwa kwa ine chifukwa cha nzeru ndili nayo yakuposa wina aliyense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma chinsinsi ichi chavumbulutsidwa kwa ine, si chifukwa chakuti ndili ndi nzeru zochuluka kuposa anthu ena onse, koma kuti mfumu mudziwe tanthauzo la maloto anu ndi kuti muzindikire maganizo amene anali mu mtima mwanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine, cinsinsi ici sicinabvumbulutsidwa kwa ine cifukwa ca nzeru ndiri nayo yakuposa wina ali yense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu.