Daniel 2:31 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu mfumu munapenya ndi kuona fano lalikulu. Fanoli linali lalikulu, ndi kunyezimira kwake kunaposa; linali kuima popenyana ndi inu, ndi maonekedwe ake anali oopsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu mfumu, munaona chinthu chowumba chachikulu chimene chinayima pamaso panu. Chowumbachi chinali chonyezimira mʼmaonekedwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu mfumu munapenya ndi kuona fano lalikuru. Fanoli linali lalikuru, ndi kunyezimira kwace kunaposa; linali kuima popenyana ndi inu, ndi maonekedwe ace anali oopsa,