Daniel 2:40 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ufumu wachinai udzakhala wolimba ngati chitsulo, popeza chitsulo chiphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga chitsulo chiswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pomaliza, padzakhala ufumu wachinayi, wolimba ngati chitsulo popeza chitsulo chimaphwanya ndi kutikita chilichonse. Ndipo monga chitsulo chimaphwanya zinthu ndikuteketeratu, choncho udzawononga ndi kuphwanya maufumu ena onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ufumu wacinai udzakhala wolimba ngati citsulo, popeza citsulo ciphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga citsulo ciswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa.