Daniel 2:45 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera chitsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golide; Mulungu wamkulu wadziwitsa mfumu chidzachitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwake kwakhazikika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Limeneli ndilo tanthauzo la masomphenya a mwala umene unagamuka pa phiri, koma osati ndi manja a anthu; mwala umene unaphwanya chitsulo, mkuwa, dongo, siliva ndi golide mʼtizidutswa. “Mulungu wamkulu wakuonetsani mfumu chimene chidzachitika kutsogolo. Malotowo ndi woona ndipo tanthauzo lake ndi lodalirika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera citsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golidi; Mulungu wamkuru wadziwitsa mfumu cidzacitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwace kwakhazikika.