Daniel 2:48 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu inasandutsa Daniele wamkulu, nimpatsa mphatso zazikulu zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babiloni; nakhala iye kazembe wamkulu wa anzeru onse a ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mfumu inamukweza Danieli ndi kumupatsa mphatso zambiri. Anamuyika kuti akhale wolamulira chigawo chonse cha Babuloni ndi kutinso akhale woyangʼanira anthu ake onse anzeru.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu inasandutsa Danieli wamkuru, nimpatsa mphatso zazikuru zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babulo; nakhala iye kazembe wamkuru wa anzeru onse a ku Babulo.