Daniel 2:5 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Niyankha mfumu, niti kwa Ababiloni, Chandichokera chinthuchi; mukapanda kundidziwitsa lotoli ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zanu zidzayesedwa dzala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inayankha alawuliwo kuti, “Zimene ndatsimikiza kuchita ndi izi: Ngati inu simundifotokozera zimene ndalota ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli ndipo nyumba zanu ndidzazisandutsa bwinja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Niyankha mfumu, niti kwa Akasidi, Candicokera cinthuci; mukapanda kundidziwitsa lotoli ndi tanthauzo lace, mudzadulidwa nthuli nthuli, ndi nyumba zanu zidzayesedwa dzala.