Daniel 2:9 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mukapanda kundidziwitsa lotoli, mlandu wanu ndi umodzi; popeza mwapanganiranatu mau onama ndi oipa, kuwanena pamaso panga, mpaka idzasanduka nyengo; chifukwa chake mundifotokozere lotoli, momwemo ndidzadziwa kuti mudzandidziwitsa kumasulira kwake komwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati simundiwuza zimene ndalota, chilango chake ndi chimodzi. Inu mwagwirizana kuti mundiwuze ine bodza ndi chinyengo ndi kuyembekeza kuti ine ndisintha. Tsono mundiwuze zimene ndalota, ndipo ine ndidzadziwa kuti mukhoza kunditanthauzira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mukapanda kundidziwitsa lotoli, mlandu wanu ndi umodzi; popeza mwapanganiranatu mau onama ndi oipa, kuwanena pamaso panga, mpaka idzasanduka nyengo; cifukwa cace mundifotokozere lotoli, momwemo ndidzadziwa kuti mudzandidziwitsa kumasulira kwace komwe.