Daniel 3:12 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Alipo Ayuda amene munawaika ayang'anire ntchito ya dera la ku Babiloni, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amuna awa, mfumu, sanasamalire inu, satumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma alipo Ayuda ena Sadirake, Mesaki ndi Abedinego amene munawayika kuti ayangʼanire ntchito ya dera la ku Babuloni. Anthu amenewa sakumvera inu mfumu. Iwo sakutumikira milungu yanu kapena kulambira fano la golide limene munaliyimikalo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Alipo Ayuda amene munawaika ayang'anire nchito ya dera la ku Babulo, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, amuna awa, mfumu, sanasamalira inu, satumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.