Daniel 3:15 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukavomereza tsono, pakumva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, chabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu amene adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano ngati muli okonzeka kulambira ndi kupembedza fano ndinalipanga, mukangomva kulira kwa lipenga chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muchita bwino. Koma ngati simulipembedza, mudzaponyedwa mʼnganjo ya moto. Nanga ndi mulungu uti amene adzatha kukupulumutsani mʼmanja anga?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukabvomereza tsono, pakumva mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ndi ngoli, ndi zoyimbitsa ziri zonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, cabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu amene adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?