Daniel 3:28 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu waowao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Nebukadinezara anati, “Atamandike Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, amene anatumiza mngelo wake ndi kupulumutsa atumiki ake! Iwo anakhulupirira Iye ndi kunyozera lamulo la mfumu ndipo anali okonzeka kutaya moyo wawo koposa kutumikira kapena kupembedza mulungu wina aliyense wosakhala Mulungu wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, amene anatuma mthenga wace, napulumutsa atumiki ace omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu wao wao.