Daniel 3:29 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uliwonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, adzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ndikulamula kuti anthu a mitundu ina kaya chiyankhulo china chili chonse amene anganyoze Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego adulidwe nthulinthuli ndipo nyumba zawo ndidzagwetsa ndi kusandutsa bwinja, popeza palibe Mulungu amene akhoza kupulumutsa mʼnjira yotere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uli wonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, adzadulidwa nthuli nthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.