Daniel 4:12 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zinachuluka, ndi m'menemo munali zakudya zofikira onse, nyama za kuthengo zinatsata mthunzi wake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinafatsa m'thambi zake, ndi nyama zonse zinadyako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masamba ake anali okongola, zipatso zinali zochuluka, ndipo mu mtengomo munali chakudya chokwanira anthu onse. Zirombo zakuthengo zimapeza mthunzi mʼmunsi mwake, ndipo mbalame zamlengalenga zimakhala pa nthambi zake: Cholengedwa chilichonse chinkadya za mu mtengowu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masamba ace anali okoma, ndi zipatso zace zinacuruka, ndi m'menemo munali zakudya zofikira onse, nyama za kuthengo zinatsata mthunzi wace, ndi mbalame za m'mlengalenga zinafatsa m'thambi zace, ndi nyama zonse zinadyako.