Daniel 4:15 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma siyani chitsa ndi mizu yake m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo; nchokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama zili m'machire a m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma musiye tsinde ndi mizu yake mʼnthaka. Tsindelo mulimange maunyolo a chitsulo ndi mkuwa, zikhalebe mʼnthaka, nʼkudya udzu mʼmunda. “ ‘Mumulole iye anyowe ndi mame akumwamba, ndipo iye akhale ndi nyama pakati pa zomera za mʼnthaka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma siyani citsa ndi mizu yace m'nthaka, comangidwa ndi mkombero wa citsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo; ncokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lace likhale pamodzi ndi nyama ziri m'macire a m'dziko.