Daniel 4:18 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Loto ili ndinaliona ine mfumu Nebukadinezara; ndipo iwe, Belitesazara, undifotokozere kumasulira kwake, popeza anzeru onse a m'ufumu wanga sakhoza kundidziwitsa kumasulira kwake; koma iwe ukhoza, popeza mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Amenewa ndi maloto amene ine, mfumu Nebukadinezara, ndinalota. Tsopano Belitesezara, undifotokozere tanthauzo lake, popeza palibe mwa anthu anzeru a mu ufumu wanga amene angathe kunditanthauzira. Koma iwe ukhoza, chifukwa mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Loto ili ndinaliona ine mfumu Nebukadinezara; ndipo iwe, Belitsazara, undifotokozere kumasulira kwace, popeza anzeru onse a m'ufumu wanga sakhoza kundidziwitsa kumasulira kwace; koma iwe ukhoza, popeza mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera.