Daniel 4:19 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Danieli, amene amatchedwa Belitesezara, anavutika mu mtima kwambiri kwa kanthawi, ndipo anasautsidwa mʼmaganizo ake. Choncho mfumu inati, “Belitesezara usalole malotowa kapena tanthauzo lake likuopse.” Belitesezara anayankha kuti, “Mbuye wanga, ndikanakonda malotowa akanakhudza adani anu okha, ndi tanthauzo lake kwa iwo okusautsani!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Danieli, dzina lace ndiye Belitsazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ace. Mfumu inayankha, niti, Belitsazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwace. Belitsazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwace kwa iwo akuutsana nanu.