Daniel 4:21 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
umene masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zochuluka, ndi m'menemo munali chakudya chofikira onse, umene nyama za kuthengo zinakhala pansi pake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinapeza pokhala pao pa nthambi yake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mtengo umene masamba ake anali okongola ndiponso unali ndi zipatso zochuluka zokwanira kudya anthu onse a dziko lapansi. Mtengowu unkapereka mthunzi ku zirombo zonse zakuthengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinayika zisa pa nthambi zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
umene masamba ace anali okoma, ndi zipatso zace zocuruka, ndi m'menemo munali cakudya cofikira onse, umene nyama za kuthengo zinakhala pansi pace, ndi mbalame za m'mlengalenga zinapeza pokhala pao pa nthambi yace;