Daniel 4:25 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, nizidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mudzachotsedwa pakati pa anthu ndipo mudzakhala ndi nyama zakuthengo; mudzadya udzu monga ngʼombe ndi kunyowa ndi mame akumwamba. Zaka zisanu ndi ziwiri zidzadutsa mpaka mudzavomereze kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye mwini ulamuliro pa ma ufumu a anthu, ndipo amawapereka kwa aliyense amene Iye wafuna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti adzakuingitsani kukucotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, nizidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna mwini.