Daniel 4:27 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani machimo anu ndi kuchita chilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kuchitira aumphawi chifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake mfumu, chikukomereni kulandira malangizo anga: Lekani machimo ndipo muzichita zabwino, lekani mphulupulu zanu ndipo muzikomera mtima anthu opsinjika. Nʼkutheka kuti mtendere wanu udzapitirira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani macimo anu ndi kucita cilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kucitira aumphawi cifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.