Daniel 4:33 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nthawi yomweyo anachitika mau awa kwa Nebukadinezara; anamuinga kumchotsa kwa anthu; nadya udzu ngati ng'ombe iye, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba, mpaka tsitsi lake lidamera ngati nthenga za chiombankhanga ndi makadabo ake ngati makadabo a mbalame.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo zonse zimene zinanenedwa zokhudza Nebukadinezara zinakwaniritsidwa. Iye anachotsedwa pakati pa anthu ndipo ankadya udzu ngati ngʼombe. Thupi lake linanyowa ndi mame akumwamba mpaka tsitsi lake linakula ngati nthenga za chiwombankhanga ndi zikhadabo ngati zikhadabo za mbalame.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nthawi yomweyo anacitika mau awa kwa Nebukadinezara; anamuinga kumcotsa kwa anthu; nadya udzu ngati ng'ombe iye, ndi thupi lace linakhathamira ndi mame a kumwamba, mpaka tsitsi lace lidamera ngati nthenga za ciombankhanga ndi makadabo ace ngati makadabo a mbalame.