Daniel 4:34 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwomibadwo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pomaliza pa zaka zimenezo ine, Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndipo nzeru zanga zinabwereramo. Kenaka ndinatamanda Wammwambamwamba; ndinamupatsa ulemu ndi kumulemekeza Iye amene akhala nthawi zonse. Ulamuliro wake ndi ulamuliro wa nthawi zonse; ufumu wake udzakhala ku mibadomibado.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumcitira ulemu Iye wokhala cikhalire; pakuti kulamulira kwace ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wace ku mibadwo mibadwo;