Daniel 4:35 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi okhala pa dziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse a dziko lapansi ali chabe pamaso pake. Pakati pa angelo akumwamba ndi anthu a dziko lapansi palibe amene akhoza kumuletsa Mulungu kuchita zimene afuna. Kapena kunena kwa Iye kuti, “Kodi mwachita chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi okhala pa dziko lapansi onse ayesedwa acabe; ndipo Iye acita mwa cifunito cace m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lace, kapena wakunena naye, Mucitanji?