Daniel 4:36 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nthawi yomweyi nzeru zanga zinandibwerera, ndi chifumu changa ndi kunyezimira kwanga zinandibwerera, kuti uonekenso ulemerero wa ufumu wanga; ndi mandoda anga ndi akulu anga anandifuna; ndipo ndinakhazikika m'ufumu wanga, Iye nandionjezeranso ukulu wochuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi yomweyo nzeru zanga zinabwereramo. Ndinalandiranso ulemu wanga ndi ufumu wanga. Nduna ndi akalonga anga anandilandiranso. Ndipo anandibwezera ufumu wanga ndi kukhalanso wamphamvu kuposa kale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nthawi yomweyi nzeru zanga zinandibwerera, ndi cifumu canga ndi kunyezimira kwanga zinandibwerera, kuti uonekenso ulemerero wa ufumu wanga; ndi mandoda anga ndi akuru anga anandifuna; ndipo ndinakhazikika m'ufumu wanga, Iye nandioniezeranso ukulu wocuruka.