Daniel 4:37 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano ine Nebukadinezara, ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba chifukwa zonse zimene amachita ndi zoyenera ndipo njira zake zonse ndi zachilungamo. Ndipo onse amene amayenda modzikuza adzawatsitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti nchito zace zonse nzoona, ndi njira zace ciweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwacepetsa.