Daniel 5:12 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza m'Daniele yemweyo, amene mfumu adamutcha Belitesazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi chidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa ndi kumasula mfundo. Amuitane Daniele tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu ameneyu dzina lake ndi Danieli, koma mfumu inamutcha Belitesezara ndipo ali ndi nzeru zapadera, ndi wodziwa ndi kuzindikira zinthu, ndiponso luso lakutanthauzira maloto, kufotokozera miyambi ndi kuthetsa mavuto osautsa. Muyitaneni Danieli, ndipo adzakuwuzani chomwe mawuwa akutanthauza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza m'Danieli yemweyo, amene mfumu adamucha Belitsazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi cidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa, ndi kumasula mfundo. Amuitane Danieli tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.