Daniel 5:17 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anayankha Daniele, nati kwa mfumu, Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzawerengera mfumu lembalo, ndi kumdziwitsa kumasulira kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Danieli anayankha mfumu kuti, “Inu musunge mphatso zanuzo kwa inu nokha ndipo mupereke mphothoyo kwa wina aliyense. Komabe ine ndi kuwerengerani malembawa mfumu; ndikukuwuzani tanthauzo lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anayankha Danieli, nati kwa mfumu, Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzawerengera mfumu lembalo, ndi kumdziwitsa kumasulira kwace.