Daniel 5:19 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo chifukwa cha ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, amanenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pake; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha udindo waukulu umene anapatsidwanso, anthu onse ndi mitundu ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana ankanjenjemera ndikumuopa iye. Amene mfumu inafuna anawaphadi; amene inafuna kuwasunga, inawasunga; amene inafuna kuwakweza, inawakweza; ndipo amene inafuna kuwatsitsa, inawatsitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo cifukwa ca ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, a manenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pace; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.