Daniel 5:21 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anamuinga kumchotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wake unasandulika ngati wa nyama za kuthengo, ndi pokhala pake mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, nauikira aliyense Iye afuna mwini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyo inachotsedwa pakati pa anthu ndi kupatsidwa mtima ngati wa nyama; inakhala pamodzi ndi abulu akutchire ndi kudya udzu ngati ngʼombe; ndipo thupi lake linanyowa ndi mame akumwamba, mpaka pamene anavomereza kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye wolamulira maufumu a anthu ndipo amawupereka kwa aliyense amene Iye wafuna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo anamuinga kumcotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wace unasandulika ngati wa nyama za kuthengo, ndi pokhala pace mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lace linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, nauikira ali yense Iye afuna mwini.