Daniel 5:7 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nifuulitsa mfumu abwere nao openda, Ababiloni, ndi alauli. Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babiloni, Aliyense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwake, adzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nadzakhala wolamulira wachitatu m'ufumuwu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inafuwula kuyitana owombeza, alawuli ndi amawula kuti abwere. Ndipo anawawuza anthu anzeru a ku Babuloni kuti, “Aliyense amene awerenge malembawa ndi kundiwuza tanthauzo lake adzavekedwa chovala cha pepo ndi mkanda wa golide udzavekedwa mʼkhosi mwake, ndipo adzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nipfuulitsa mfumu abwere nao openda, Akasidi, ndi alauli, Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babulo, Ali yense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwace, adzabvekedwa cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwace, nadzakhala wolamulira wacitatu m'ufumuwu.