Daniel 6:12 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za choletsacho cha mfumu, Kodi simunatsimikiza choletsacho, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Choona chinthuchi, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero iwo anapita kwa mfumu ndipo anayankhula naye za lamulo lake kuti, “Kodi simunasindikize lamulo lakuti pa masiku makumi atatu otsatirawa aliyense amene apemphera kwa mulungu wina aliyense kapena kwa munthu kupatula kwa inu mfumu, adzaponyedwa mʼdzenje la mikango?” Mfumu inayankha kuti, “Lamulo lilipobe monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sangathe kusinthika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za coletsaco ca mfumu, Kodi simunatsimikiza coletsaco, kuti ali yense akapempha kanthu kwa mulungu ali yense, kapena kwa munthu ali yense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Coona cinthuci, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika.