Daniel 6:13 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anayankha, nati pamaso pa mfumu, Daniele uja wa ana a ndende a Yuda sasamalira inu, mfumu, kapena choletsa munachitsimikizacho; koma apempha pemphero lake katatu tsiku limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka iwo anati kwa mfumu, “Danieli, amene ndi mmodzi mwa akapolo ochokera ku Yuda, sakulabadira inu mfumu, kapena lamulo limene munasindikizapo dzina lanu lija. Iye akupempherabe katatu pa tsiku.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anayankha, nati pamaso pa mfumu, Danieli uja wa ana a ndende a Yuda sasamalira inu, mfumu, kapena coletsa munacitsimikizaco; koma apempha pemphero lace katatu tsiku limodzi.