Daniel 6:24 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa lamulo la mfumu, anthu onse amene ananeneza Danieli aja anagwidwa ndi kukaponyedwa mʼdzenje la mikango, pamodzi ndi akazi awo ndi ana awo. Ndipo asanafike pansi pa dzenjelo, mikango inawawakha ndi mphamvu ndi kuteketa mafupa awo onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Danieli, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.