Daniel 6:4 — Compare Translations

3 translations compared side by side

Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha ichi, anzake ndi akalonga anayesa kupeza zifukwa zomutsutsira Danieli pa kayendetsedwe ka ntchito za dzikolo, koma sanapeze cholakwa chilichonse. Iwo sanapeze chinyengo mwa iye, chifukwa anali wokhulupirika ndipo sankachita chinyengo kapena kutayirira ntchito.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola cifukwa Danieli, kunena za ufumuwo; koma sanakhoza kupeza cifukwa kapena colakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo sanaona cosasamala kapena colakwa ciri conse mwa iye.